2 Samuel 16:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta wakulipsira chifukwa chakuti udapha onse a banja la Saulo, nulanda ufumu wake. Ndipotu Chauta wapereka ufumuwo kwa mwana wako Abisalomu. Ona, kutha kwako nkumeneku, pakuti iweyo ndiwe wopha anthu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Saulo, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwake; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, chifukwa uli munthu wa mwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wakubwezera chifukwa cha magazi onse amene unakhetsa pa nyumba ya Sauli, yemwe iwe ukulamulira mʼmalo mwake. Yehova wapereka ufumu kwa mwana wako Abisalomu. Ndipo ona mathero ako ndi amenewa chifukwa ndiwe munthu wopha anthu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wabwezera pa iwe mwazi wonse wa nyumba ya Sauli, amene iwe wakhala mfumu m'malo mwace; ndipo Yehova wapereka ufumuwo m'dzanja la Abisalomu mwana wako; ndipo ona, wagwidwa m'kuipa kwako kwa iwe wekha, cifukwa uli munthu wa mwazi.