2 Samuel 16:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa mfumu kuti, “Bwanji mukulola galu wakufayu kuti akutukwaneni chotere, inu mbuyanga mfumu? Mundilole ndikamdule pa khosi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Galu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anati kwa mfumu, “Nʼchifukwa chiyani galu wakufa uyu akutukwana mbuye wanga mfumu? Ndiloleni ndipite kuti ndikadule mutu wake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Abisai mwana wa Zeruya ananena ndi mfumu, Garu wakufa uyu atukwaniranji mbuye wanga mfumu? Mundilole ndioloke ndi kudula mutu wace.