2 Samuel 17:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono ngakhale munthu wolimba mtima ngati mkango adzaguluka m'nkhongono. Paja Aisraele onse akudziŵa kuti bambo wanu ndi munthu wamphamvu, ndipo kuti anthu amene ali nawowo ngolimba mtima.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wake ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisraele onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono ngakhale msilikali wolimba mtima kwambiri, amene mtima wake uli ngati wa mkango, adzagwidwa ndi mantha aakulu pakuti Aisraeli akudziwa kuti abambo anu ndi ankhondo ndipo kuti iwo amene ali nawo ndi anthu olimba mtima.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngakhale ngwazi imene mtima wace ukunga mtima wa mkango idzasungunuka konse, pakuti Aisrayeli onse adziwa atate wanu kuti ndiye munthu wamphamvu, ndi iwo ali naye ndiwo ngwazi.