2 Samuel 17:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Ine malangizo anga ndi aŵa: Aisraele onse adzasonkhane kwa inu kuno, kuyambira ku Dani mpaka ku Beereseba, adzakhale ochuluka ngati mchenga wa m'mbali mwa nyanja. Ndipo inu nomwe mudzapite nawo ku nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisraele onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mchenga uli panyanja kuchuluka kwao; ndi kuti mutuluke kunkhondo mwini wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Kotero ine ndikukulangizani kuti: Aisraeli onse, kuchokera ku Dani mpaka ku Beeriseba; ochuluka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja, asonkhane kwa inu ndipo muwatsogolera kupita ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma uphungu wanga ndiwo kuti musonkhanitse Aisrayeli onse kwa inu kuyambira ku Dani kufikira ku Beereseba, monga mcenga uli panyanja kucuruka kwao; ndi kuti muturuke kunkhondo mwini wace.