2 Samuel 17:14 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atamva zimenezi Abisalomu ndi Aisraele onse adati, “Malangizo koma aŵa a Husai Mwarikiyu, osati a Ahitofele aja ai.” Zidatero chifukwa Chauta ndiye adaakonza kuti malangizo abwino a Ahitofele alephereke, zinthu zisamuyendere bwino Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israele anati, Uphungu wa Husai Mwariki uposa uphungu wa Ahitofele. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofele kuti Yehova akamtengere Abisalomu choipa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu ndi ankhondo ena onse a Israeli anati, “Malangizo a Husai Mwariki ndi abwino kuposa a Ahitofele.” Pakuti Yehova anatsimikiza kutsutsa malangizo onse abwino a Ahitofele ndi cholinga choti zimuvute Abisalomu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu ndi anthu onse a Israyeli anati, Uphungu wa Husai M-ariki uposa uphungu wa Ahitofeli. Pakuti kunaikidwa ndi Yehova kutsutsa uphungu wabwino wa Ahitofeli kuti Yehova akamtengere Abisalomucoipa.