2 Samuel 17:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kenaka Husai adauza Zadoki ndi Abiyatara, ansembe aja, kuti, “Zimene Ahitofele adaalangiza Abisalomu ndi atsogoleri a Aisraele ndi izi, izi. Koma ineyo ndaŵalangiza izi, izi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Husai anawuza ansembe Zadoki ndi Abiatara kuti, “Ahitofele analangiza Abisalomu ndi akuluakulu a Israeli zakuti, koma ine ndawalangiza kuchita zakutizakuti.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abyatara ansembewo, Ahitofeli anapangira Abisalomu ndi akuru a Israyeli zakuti zakuti; koma ine ndinapangira zakuti zakuti.