2 Samuel 17:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye inu tsono mutumize mau mwamsanga kwa Davide omuuza kuti asagone pa madooko a Yordani ku chipululu. Koma mwa njira iliyonse, aoloke ndithu, kuti iye pamodzi ndi anthu onse amene ali naye angagwidwe ndi kuphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti Musagona usiku uno pa madooko a kuchipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsopano tumizani wamthenga msangamsanga kuti akamuwuze Davide kuti, ‘Musakagone powolokera Yorodani ku chipululu koma mukawoloke. Mukapanda kutero, mfumu ndi anthu onse amene ali naye adzaphedwa.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace tsono mutumize msanga nimuuze Davide kuti, Musagona usiku uno pa madooko a kucipululu, koma muoloke ndithu, kuti mfumu ingamezedwe ndi anthu onse amene ali naye.