2 Samuel 17:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma tsiku lina mnyamata wina adaŵaona, nakauza Abisalomu. Choncho Yonatani ndi Ahimaazi adathaŵa mofulumira, nakafika ku Bahurimu ku nyumba ya munthu wina, amene anali ndi chitsime pakhomo pake. Aŵiriwo adatsikira m'chitsimemo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anachoka msanga onse awiri, nafika kunyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali nacho chitsime pabwalo pake; ndipo anatsikira m'menemo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mnyamata wina anawaona ndipo anakawuza Abisalomu. Kotero anthu awiriwo anachoka mofulumira ndipo anapita ku nyumba ya munthu wina ku Bahurimu. Iye anali ndi chitsime ku mpanda kwake ndipo iwo analowamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mnyamata wina anawaona nauza Abisalomu; ndipo ajawo anacoka msanga onse awiri, nafika ku nyumba ya munthu ku Bahurimu, amene anali naco citsime pabwalo pace; ndipo anatsikira m'menemo.