2 Samuel 17:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mkazi wa munthu uja adatenga chivundikiro, nachiika pamwamba pa chitsimecho, nkuyanikapo tirigu, kotero kuti chitsimecho sichinkadziŵika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mkazi anatenga chivundikiro nachiika pakamwa pa chitsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sichinadziwika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mkazi wake anatenga chophimba ndipo anachiyika pamwamba pa chitsimecho nawazapo tirigu. Palibe amene anadziwa chilichonse za izi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mkazi anatenga cibvundikilo naciika pakamwa pa citsime, napapasapo lipande la tirigu; momwemo sicinadziwika.