2 Samuel 17:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a Abisalomu atabwera kwa mkaziyo kunyumba kuja, adamufunsa kuti, “Kodi mwaonako Ahimaazi ndi Yonatani pano?” Mkazi uja adaŵayankha kuti, “Amenewo aoloka mtsinjewu.” Koma ataŵafunafuna, osaŵapeza, ankhondowo adabwerera ku Yerusalemu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Yonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kunka ku Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu a Abisalomu atafika kwa mkaziyo pa nyumbapo anafunsa kuti, “Kodi Ahimaazi ndi Yonatani ali kuti?” Mkaziyo anawayankha kuti, “Awoloka mtsinje.” Anthuwo anafunafuna koma sanapeze munthu, kotero anabwerera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anyamata a Abisalomu anafika kunyumba kwa mkaziyo; nati, Ali kuti Ahimaazi ndi Jonatani? Ndipo mkaziyo ananena nao, Anaoloka kamtsinje kamadzi. Ndipo atawafunafuna, osawapeza, anabwerera kumka ku Yerusalemu.