2 Samuel 17:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahitofele ataona kuti anthu sadatsate malangizo ake aja, adakwera bulu wake, napita kwao ku mzinda wake. Tsono adakonza zonse za m'nyumba mwake, nadzikhweza. Motero adafa, ndipo adaikidwa m'manda a bambo wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ahitofele ataona kuti malangizo ake sanatsatidwe, iye anakwera bulu wake napita ku mzinda wa kwawo ku nyumba yake. Iye anakonza mʼnyumba mwakemo ndi kudzimangirira. Kotero anafa nayikidwa mʼmanda a abambo ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahitofeli, pakuona kuti sautsata uphungu wace anamanga buru wace, nanyamuka, nanka kumudzi kwao, nakonza za pa banja lace, nadzipacika, nafa, naikidwa m'manda a atate wace.