2 Samuel 17:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Abisalomu adaaika Amasa kuti akhale mtsogoleri wa ankhondo m'malo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wina dzina lake Yetere Mwismaele, amene adaakwatira Abigala, mwana wa Nahasi, mlongo wa Zeruya amake a Yowabu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yowabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lake Yetere Mwismaele, amene analowa kwa Abigaile, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Abisalomu anasankha Amasa kukhala mkulu wa ankhondo mʼmalo mwa Yowabu. Amasa anali mwana wa munthu wotchedwa Itira Mwisraeli amene anakwatira Abigayeli mwana wa Nahasi mlongo wake wa Zeruya, amayi ake a Yowabu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu anaika Amasa, kazembe wa khamulo, m'malo a Yoabu. Koma Amasayu ndiye mwana wa munthu dzina lace Itra M-israyeli, amene analowa kwa Abigayeli, mwana wamkazi wa Nahasi, mlongo wa Zeruya, amai a Yoabu.