2 Samuel 17:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Husai atabwera kwa Abisalomu, Abisalomuyo adamuuza kuti, “Zimene wanena Ahitofele nzimenezi, kodi tichitedi monga m'mene watilangiziramo? Ngati si choncho, iweyo utiwuze chochita.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofele analankhula mau akuti; tichite kodi monga mwa kunena kwake? Ngati iai, unene ndiwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Husai atabwera kwa iye, Abisalomu anati, “Ahitofele wapereka malangizo ake. Kodi tichite zimene wanena? Ngati sichoncho, tiwuze maganizo ako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pakufika Husai kwa Abisalomu, Abisalomuyo ananena naye, Ahitofeli analankhula mau akuti; ticite kodi monga mwa kunena kwace? ngati iai, unene ndiwe.