2 Samuel 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mukudziŵa kuti bambo wanu ngwamphamvu, anthu akenso ngamphamvu, ndipo kuti onse ngokwiya ngati zimbalangondo zolandidwa ana ku thengo. Kuwonjezera pamenepo, bambo wanu ndi katswiri wa nkhondo. Sangagone pamodzi ndi anthu ake ankhondo usiku.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ake kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga chimbalangondo chochilanda ana ake kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mukudziwa bwino abambo anu ali ndi ankhondo awo. Iwo ndi anthu ankhondo komanso ndi woopsa ngati chimbalangondo chimene chalandidwa ana ake. Kuwonjezera apa abambo anu ndi katswiri wa nkhondo. Iwo sanagone pamodzi ndi asilikali awo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Husai anatinso, Mudziwa atate wanu ndi anthu ace kuti ndizo ngwazi, ndipo ali ndi mitima yowawa monga cimbalangondo cocilanda ana ace kuthengo; ndipo atate wanu ali munthu wodziwa nkhondo, sadzagona pamodzi ndi anthu.