2 Samuel 17:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Onani, ngakhale tsopano lino akubisala m'phanga lina, kapena ku malo ena ake. Motero ena mwa anthu anu atangophedwa poyamba pomwe, aliyense amene adzamve adzanena kuti, ‘Anthu amene ankatsata Abisalomu aphedwa.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, aliyense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Onani, ngakhale tsopano lino abisala mʼphanga lina ku malo ena ake. Ngati iwo atayamba kuthira nkhondo asilikali anu, aliyense amene adzamve zimenezi adzati, ‘Gulu lalikulu lankhondo lotsatira Abisalomu laphedwa.’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Onani, tsopanoli alikubisala kudzenje kapena kwina; ndipo kudzali poyamba kugwa ena, ali yense wakumva adzanena, Alikuphedwa anthu otsata Abisalomu.