2 Samuel 18:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Munthu wina ataona zimenezo, adauza Yowabu kuti, “Ndamuwona Abisalomu ali lendee mu mtengo wa thundu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yowabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mmodzi mwa asilikali ataona zimenezi, anamuwuza Yowabu kuti, “Ine ndamuona Abisalomu ali lende mu mtengo wa thundu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munthu wina anamuona, nauza Yoabu, nati, Onani, ndaona Abisalomu ali lende pathundu.