2 Samuel 18:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma munthuyo adauza Yowabu kuti, “Ngakhale ndikadalandira m'manja mwangamu ndalama zasiliva zokwanira 1,000, sindikadasamula dzanja langa kuti ndiphe mwana wa mfumu. Paja mfumu idakulamulani inu ndi Abisai ndi Itai, ife tilikumva, kuti, ‘Mumtchinjirize mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma munthuyo anayankha kuti, “Ngakhale atandipatsa mʼmanja mwanga ndalama zasiliva 1,000, sindingatambasule dzanja langa kupha mwana wa mfumu. Ife tikumva, mfumu inalamula inu Abisai ndiponso Itai kuti, ‘Mutetezeni mnyamatayo Abisalomu chifukwa cha ine!’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Munthuyo nanena ndi Yoabu, Ndingakhale ndikalandira ndarama cikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi ltai, kuti, Cenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.