2 Samuel 18:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahimaazi, mwana wa Zadoki, adati, “Imani ndithamange ndikauze mfumu nkhani yokondwetsayi yakuti Chauta waipulumutsa mfumuyo kwa adani ake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera chilango adani ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, “Ndiloleni ndithamange ndi kukapereka uthenga kwa mfumu kuti Yehova wayipulumutsa mʼdzanja la adani ake.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pomwepo Ahimaazi mwana wa Zadoki anati, Ndithamange nditengere mfumu mau kuti Yehova wabwezera cilango adani ace.