2 Samuel 18:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo Davide adatumiza gulu lankhondo ataligaŵa patatu, chigawo chimodzi cholamulidwa ndi Yowabu, china cholamulidwa ndi Abisai, mwana wa Zeruya, mng'ono wake wa Yowabu, china cholamulidwa ndi Itai Mgiti. Tsono mfumu idauza anthuwo kuti, “Inenso ndipita nao.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anatumiza asilikaliwo atawagawa patatu: gulu loyamba limalamulidwa ndi Yowabu, gulu lachiwiri limalamulidwa ndi Abisai ndipo gulu lachitatu limalamulidwa ndi Itai Mgiti. Mfumu inawuza asilikaliwo kuti, “Inenso ndipita nanu ndithu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yoabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yoabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzaturuka limodzi ndi inu.