2 Samuel 18:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Yowabu adauza Ahimaaziyo kuti, “Iwe usakanene zimenezi lero. Ukanene zimenezi tsiku lina, koma lero usakanene mbiri iliyonse, chifukwa mwana wa mfumu waphedwa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yowabu anamuwuza iye kuti, “Iwe si amene uti ukanene zimenezi lero. Ukapereka uthenga nthawi ina, koma usatero lero, chifukwa mwana wa mfumu wafa.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yoabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, cifukwa mwana wa mfumu wafa.