2 Samuel 18:23 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ahimaazi adati, “Zitanizitani, ine ndithamanga ndithu.” Apo Yowabu adamuuza kuti, “Chabwino, pita.” Choncho Ahimaazi adathamanga, kudzera njira yakuchigwa, nkumubzola Mkusi uja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange. Iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kuchigwa, napitirira Mkusi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anati, “Zivute zitani ine ndikufuna kuti ndipite.” Choncho Yowabu anati “Pita!” Ndipo Ahimaazi anathamanga kudzera njira ya ku chigwa ndipo anamupitirira Mkusi uja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma ngakhale kotero, anati iye, Ndithamange, iye nanena naye, Thamanga. Ndipo Ahimaazi anathamanga njira ya kucigwa, napitirira Mkusi.