2 Samuel 18:24 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziŵiri, chakubwalo ndi cham'kati. Mlonda adakwera pa khoma nakaimirira pa denga la chipata. Adati atayang'ana, adaona munthu akuthamanga yekhayekha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la chipata cha kulinga, natukula maso ake, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nthawi imeneyo nʼkuti Davide atakhala pakati pa zipata ziwiri, chakubwalo ndi chamʼkati. Mlonda anakwera pa khoma nakayimirira pa denga la chipata. Anati atayangʼana, anaona munthu akuthamanga yekhayekha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Davide anakhala pakati pa zipata ziwiri; ndipo mlonda anakwera pa tsindwi la cipata ca kulinga, natukula maso ace, napenya; naona munthu alikuthamanga yekha.