2 Samuel 18:26 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlondayo adaona munthu winanso akuthamanga. Ndipo adafuulira munthu wapachipata nati, “Onani, pali munthu winanso akuthamanga yekhayekha.” Apo mfumu idati, “Iyeyonso akubwera ndi nkhani yabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakuchipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, Iyenso abwera ndi mau.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlonda uja anaonanso munthu wina akuthamanga, ndipo anayitana woyangʼanira pa chipata, “Taona, munthu winanso akuthamanga ali yekha!” Mfumu inati, “Iye akubweretsanso nkhani yabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mlondayo anaona munthu wina wothamanga; mlonda naitana wakucipata nanena, Taona munthu wina wakuthamanga yekha. Ndipo mfumu inati, iyenso abwera ndi mau.