2 Samuel 18:27 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mlonda uja adati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi m'mene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu idati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki. Ndipo mfumu inati, Iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mlonda uja anati, “Munthu akuthamanga patsogoloyo, kathamangidwe kake kakufanafana ndi mmene amathamangira Ahimaazi, mwana wa Zadoki.” Mfumu inati, “Ameneyo ndi munthu wabwino, ndipo akubwera ndi nkhani yabwino.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mlondayo nati, Ndiyesa kuti kuthamanga kwa wapatsogoloyo kunga kuthamanga kwa Ahimaazi mwana wa Zadoki, Ndipo mfumu inati, iye ndiye munthu wabwino, alikubwera ndi mau okoma.