2 Samuel 18:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ahimaazi adafuula kwa mfumu, kuti, “Nkwabwino!” Atatero adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumu, nati, “Atamandike Chauta, Mulungu wanu, amene wapereka m'manja mwanu anthu amene adaaukira inu mbuyanga mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Ahimaazi anafuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yake pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Ahimaazi anafuwula kwa mfumu, “Zonse zili bwino!” Iye anagwada pamaso pa mfumu nkhope yake atagunditsa pansi ndipo anati, “Yehova Mulungu wathu alemekezedwe! Iye wapereka mʼdzanja lathu anthu amene anawukira inu mbuye wanga mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Ahimaazi anapfuula, nanena ndi mfumu, Mtendere. Ndipo anawerama pamaso pa mfumu ndi nkhope yace pansi, nati, Alemekezeke Yehova Mulungu wanu amene anapereka anthu akukwezera dzanja lao pa mbuye wanga mfumu.