2 Samuel 18:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idamufunsa kuti, “Kodi mwana uja Abisalomu, zinthu zamuyendera bwino?” Ahimaazi adauza mfumu kuti, “Pamene Yowabu amandituma ine, kapolo wanu, ndinaona chipiringu chachikulu cha anthu, sindikudziŵa kaya kwagwa zotani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yowabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringupiringu, koma sindinadziwa ngati kutani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inafunsa, “Kodi mnyamata uja Abisalomu watetezedwa?” Ahimaazi anayankha, “Pamene Yowabu amati azindituma ine mtumiki wanu ndinaona chipiringu cha anthu, koma sindikudziwa chinali chiyani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inati, Kodi mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Ahimaazi nayankha, Pamene Yoabu anatumiza mnyamata wa mfumu, ndiye ine mnyamata wanu, ndinaona piringu piringu, koma sindinadziwa ngati kutani.