2 Samuel 18:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma anthuwo adati, “Inuyo simupita nao, chifukwa ife tikathaŵa, adani sadzatisamala. Ngati theka la ife lifa, iwo sadzasamalako za ife. Koma inu mukuposa anthu 10,000 mwa ife. Nchifukwa chake nkwabwino kwambiri kuti inu muzingotitumizira chithandizo kuchokera kumzindako.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma anthuwo anati, Simudzatuluka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; chifukwa chake tsono nkwabwino kuti mutithandize kutuluka m'mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma anthuwo anati, “Inu musapite nafe. Ngati tidzathamangitsidwa, iwowo sadzasamala za ife. Ngakhale theka la ife litafa, iwo sadzasamalako. Koma inuyo ndinu ofunika kuposa asilikali 10,000. Nʼkwabwino kwambiri kuti inu muzititumizira chithandizo kuchokera ku mzindako.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma anthuwo anati, Simudzaturuka ndinu; pakuti tikathawa sadzatisamalira ife; ngakhale limodzi la magawo awiri a ife likafa sadzatisamalira; koma inu mulingana ndi zikwi khumi a ife; cifukwa cace tsono nkwabwino kuti mutithandize kuturuka m'mudzi.