2 Samuel 18:31 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mkusi uja nayenso adafika, ndipo adati, “Ndakutengerani uthenga wabwino, mbuyanga mfumu. Lero lino Chauta wakupulumutsani ku mphamvu za anthu onse amene ankakuukirani.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera chilango lero onse akuukira inu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Mkusi uja anafika ndipo anati, “Mbuye wanga mfumu imvani nkhani yabwino! Yehova wakupulumutsani inu lero kwa onse amene anakuwukirani.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo onani, Mkusiyo anafika, nati, Mau akuuza mbuye wanga mfumu; pakuti Yehova anabwezera cilango lero onse akuukira inu.