2 Samuel 18:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamenepo mfumu idagwidwa ndi chisoni chachikulu, nikwera ku chipinda cham'mwamba pa chipata kukalira. Tsono popita inkati, “Iwe mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu. Kalanga ine, achikhala ndidaafa ndine m'malo mwako! Iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inanthunthumira. Inapita ku chipinda cha mmwamba cha pa chipata kukalira. Pamene imapita, inkati: “Iwe mwana wanga Abisalomu! Mwana wanga! Mwana wanga Abisalomu! Zikanakhala bwino ndikanafa ndine mʼmalo mwako! Iwe Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumuyo inagwidwa cisoni, nikwera ko cipinda cosanja pa cipataco, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!