2 Samuel 18:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu idaŵauza kuti, “Chilichonse chimene chikukomereni, ndidzachita.” Choncho mfumuyo idakaimirira pambali pa chipata nthaŵi imene gulu lonse lankhondo linkatuluka mazanamazana, ndiponso zikwizikwi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzachita chimene chikomera inu. Mfumu niima pambali pa chipata, ndipo anthu onse anatuluka ali mazana, ndi zikwi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha kuti, “Ine ndichita chimene chili chokukomerani.” Kotero mfumu inayima pambali pa chipata pamene ankhondo onse amayenda mʼmagulu a anthu 100 ndi a 1,000.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanena nao, Ndidzacita cimene cikomera inu. Mfumu niima pambali pa cipata, ndipo anthu onse anaturuka ali mazana, ndi zikwi.