2 Samuel 18:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumu idalamula Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumlezere mtima mwanayo Abisalomu chifukwa cha ine.” Anthu onse adamva pamene mfumu inkalamula atsogoleri a ankhondo kunena za Abisalomu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inalamulira Yowabu, Abisai ndi Itai kuti, “Mumukomere mtima Abisalomu chifukwa cha ine.” Ndipo asilikali onse anamva pamene mfumu imalamula izi za Abisalomu kwa wolamulira aliyense.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inalamulira Yoabu nd Abisai ndi ltai, kuti, Cifukwa ca ine mucite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.