2 Samuel 18:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mwadzidzidzi Abisalomu adakumana ndi ankhondo a Davide. Abisalomuyo anali atakwera pa bulu wake, ndipo buluyo adaloŵa kunsi kwa nthambi zochindikira za mtengo wa thundu. Pamenepo Abisalomu adatsalira ali lendee, mutu wake utapanika pa nthambiyo, pamene bulu ankakwerayo adapitirira.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yake, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkulu. Ndipo mutu wake unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye inapitirira.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono zinachitika kuti Abisalomu anakumana ndi asilikali a Davide. Iye anali atakwera bulu ndipo pamene buluyo amadutsa pansi pa nthambi zambiri za mtengo wa thundu, mutu wa Abisalomu unakodwa mu mtengomo. Iye anasiyidwa atatsakamira mʼmalele, pamene bulu amene anakwerapoyo amapitirira.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu anakomana ndi anyamata a Davide. Abisalomu naberekeka pa nyuru yace, ndipo nyuruyo inapita pansi pa nthambi zolimba za thundu wamkuru. Ndipo mutu wace unakodwa ndi mtengo, iye ali lende pakati pa thambo ndi pansi ndi nyuru imene inali pansi pa iye Inapitirira.