2 Samuel 19:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Abisalomuyo amene ife tidamdzoza kuti akhale mfumu yathu, adafa ku nkhondo. Chifukwa chiyani tsono simukunena kanthu zokatenga mfumu Davide kuti abwerenso?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Chifukwa chake tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo Abisalomu amene ife tinamudzoza kuti atilamulire wafa pa nkhondo. Tsono nʼchifukwa chiyani simukunena kanthu za kubweretsanso mfumu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Abisalomu amene tinamdzoza mfumu yathu anafa kunkhondo. Cifukwa cace tsono mulekeranji kunena mau akuti abwere nayo mfumuyo?