2 Samuel 19:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mfumu Davide adatumiza mau kwa ansembe aja, Zadoki ndi Abiyatara, akuti, “Mufunse atsogoleri a ku Yuda kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mukuzengereza kwambiri osakaitenganso mfumu kuti ibwerere ku nyumba kwake, pamene Aisraele onse atumiza kale mau kwa mfumu onena kuti mfumu ibwerere kunyumba kwake?
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akulu a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu kunyumba yake? Pakuti mau a Aisraele onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo kunyumba yake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu Davide inatumiza uthenga uwu kwa ansembe Zadoki ndi Abiatara, “Funsani akuluakulu a Yuda, ‘Nʼchifukwa chiyani inu mukukhala otsiriza kuyitana mfumu ku nyumba yake yaufumu, pakuti zimene zikunenedwa mu Israeli yense zamveka kwa mfumu ndi onse amene akukhala nayo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu Davide anatumiza kwa Zadoki ndi Abyatara ansembewo, nati, Mulankhule nao akuru a Yuda, kuti, Mukhale bwanji am'mbuyo kubwera nayo mfumu ku nyumba yace? pakuti mau a Aisrayeli onse anafika kwa mfumu akuti abwere nayo ku nyumba yace.