2 Samuel 19:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu ndinu abale anga enieni. Chifukwa chiyani inuyo mukufuna kukhala otsirizira pakuiitananso mfumu?’
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu ndinu abale anga, muli fupa langa ndi mnofu wanga; chifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu ndinu abale anga enieni, mafupa anga ndi mnofu wanga. Nʼchifukwa chiyani inuyo mukukhala otsiriza kubweretsa mfumu?’
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inu ndinu abale anga, muli pfupa langa ndi mnofu wanga; cifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?