2 Samuel 19:13 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mukauze Amasa mau anga oti, ‘Kodi iwe, sindiwe mbale wanga weniweni?’ Ndithu Mulungu andilange, mpaka ndife ndithu, ngati sindikuika iwe kuti ukhale mkulu wankhondo m'malo mwa Yowabu kuyambira tsopano lino.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo munene kwa Amasa, ‘Kodi iwe si mʼbale wanga weniweni? Mulungu andilange, andilange kwambiri ngati kuyambira tsopano sukhala mtsogoleri wa ankhondo anga kulowa mʼmalo mwa Yowabu.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo munene ndi Amasa, Suli pfupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala cikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yoabu.