2 Samuel 19:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero mfumu idabwerera ku Yordani. Ndipo anthu onse a mtundu wa Yuda adafika ku Giligala kudzakumana ndi mfumu ndi kuiwolotsa Yordani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho mfumu inabwera nifika ku Yordani. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero mfumu inabwerera ndipo inakafika mpaka ku Yorodani. Tsono anthu a ku Yuda anabwera ku Giligala kuti akakumane ndi mfumu ndi kumuwolotsa Yorodani.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco mfumu inabwera nifika ku Yordano. Ndipo Ayuda anadza ku Giligala, kuti akakomane ndi mfumu, ndi kumuolotsa mfumu pa Yordano.