2 Samuel 19:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, adabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Simei mwana wa Gera, wa fuko la Benjamini wa ku Bahurimu, anabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Simeyi, mwana wa Gera, Mbenjammi, wa ku Bahurimu, anafulumira natsika pamodzi ndi anthu a Yuda kuti akakomane ndi mfumu Davide.