2 Samuel 19:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a ku Benjamini. Zibanso mtumiki uja wa m'banja la Saulo, pamodzi ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndiponso antchito ake makumi aŵiri, adathamangira ku Yordani, nakafikako isanafike mfumu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a fuko la Benjamini pamodzi ndi Ziba, wantchito wa banja la Sauli ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndi antchito ake makumi awiri. Iwo anathamangira ku Yorodani kumene kunali mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anali nao anthu cikwi cimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saul; ndi ana ace amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ace makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordano pamaso pa mfumu.