2 Samuel 19:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo adaolotsa onse a m'banja la mfumu, nachita zonse zokondweretsa mfumuyo. Tsono pamene mfumu Davide anali pafupi kuwoloka Yordani, Simei mwana wa Gera, adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna. Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kucita comkomera. Ndipo Simeyi mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordano.