2 Samuel 19:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Choncho chikondwerero cha tsikulo chidasanduka maliro kwa anthu onse, pakuti anthu adamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo kwa asilikali onse chipambano cha tsiku limenelo chinasandulika maliro, chifukwa tsiku limenelo anthu anamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cipulumutso ca tsiku lila cinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu iri ndi cisoni cifukwa ca mwana wace.