2 Samuel 19:20 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ine kapolo wanu ndikudziŵa kuti ndidalakwa. Nchifukwa chake mukuwona kuti ndabwera lero lino, ndipo m'banja lonse la Yosefe, ndayambira ndine kubwera kudzakuchingamirani inu mbuyanga mfumu.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinachimwa; chifukwa chake, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti ine mtumiki wanu ndazindikira kuti ndachimwa. Koma lero ndabwera ngati woyamba wa nyumba ya Yosefe yonse kudzakumana nanu mbuye wanga mfumu.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti mnyamata wanu ndidziwa kuti ndinacimwa; cifukwa cace, onani, ndinadza lero, ndine woyamba wa nyumba yonse ya Yosefe kutsika kuti ndikomane ndi mbuye wanga mfumu.