2 Samuel 19:22 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma Davide adayankha kuti, “Za ine zikukukhudzani bwanji, inu ana a Zeruya, kuti lero lino mukhale ngati adani anga. Kodi lero m'dziko la Israele nkuphamo munthu? Kodi sindikudziŵa kuti tsopano ndine mfumu ya Aisraele?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma Davide anati, Ndili ndi chiyani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israele lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israele lero?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Davide anayankha kuti, “Kodi inu ana a Zeruya, ndikuchitireni chiyani? Lero lino iwe wakhala mdani wanga! Kodi wina aphedwe lero mu Israeli? Kodi ine sindikudziwa kuti lero ndine mfumu mu Israeli?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma Davide anati, Ndiri ndi ciani inu, ana a Zeruya inu, kuti muzikhala akutsutsana ndi ine lero? Kodi munthu adzaphedwa m'Israyeli lero? Sindidziwa kodi kuti ndine mfumu ya Israyeli lero?