2 Samuel 19:24 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Mefiboseti, mdzukulu wa Saulo, adapita kukakumana ndi mfumu. Sadasambe m'miyendo, ndevu osameta, ndipo sadachape zovala zake kuyambira tsiku limene mfumu idachoka, mpaka tsiku limene idabwerera mwamtendere.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mefiboseti, mdzukulu wa Sauli, nayenso anabwera kudzakumana ndi mfumu. Kuyambira tsiku limene mfumu inachoka mpaka tsiku limene inabwerera mu mtendere, iye sanasambe mapazi kaya kumeta ndevu kapena kuchapa zovala zake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Mefiboseti mwana wa Sauli anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasamba mapazi ace, kapena kumeta ndebvu zace, kapena kutsuka zobvalazace kuyambira tsiku lomuka mfumukufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.