2 Samuel 19:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndiye pamene ankabwera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Iwe Mefiboseti, chifukwa chiyani sudapite nane limodzi?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Chifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene anafika kuchokera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumu inamufunsa kuti, “Nʼchifukwa chiyani sunapite nane Mefiboseti?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kunali pakufika iye ku Yerusalemu kukakomana ndi mfumu, mfumu inanena naye, Cifukwa ninji sunapita nane Mefiboseti?