2 Samuel 19:26 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mefiboseti adayankha kuti, “Ine mbuyanga mfumu, adaandilakwitsa ndi wantchito wanga. Kapolo wanune wantchitoyo ndidamuuza bwinobwino kuti, ‘Undimangire chishalo pa bulu kuti ndikwere, ndipite nawo limodzi amfumu,’ poti paja ine kapolo wanu ndine wolumala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye anayankha kuti, “Mbuye wanga mfumu, pakuti ine wantchito wanu ndine wolumala. Ndinati, ‘Andikonzere chishalo cha bulu wanga ndipo ndidzakwera kuti ndipite ndi mfumu.’ Koma Ziba wantchito wanga anandilakwitsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira buru kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndiri wopunduka.