2 Samuel 19:28 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja anthu onse a banja la bambo wanga anali oyenera kuphedwa ndi inu mbuyanga mfumu. Koma ine mtumiki wanu mudaandiika pakati pa anthu amene ankadya ndi inu pa tebulo lanu. Nanga ndingakhale ndi chiyaninso ine chimene chingandiyenereze kuti ndingadandaule kwa inu amfumu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjezere kudandaulira kwa mfumu?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti nyumba yonse ya atate wanga inali anthu oyenera imfa pamaso pa mbuye wanga mfumu; koma inu munaika mnyamata wanu pakati pa iwo akudya pa gome lanu. Kuyenera kwanga nkutaninso kuti ndikaonjeze kudandaulira kwa mfumu?