2 Samuel 19:29 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Apo mfumu idati, “Basi ndamva usaonjezenso mau ena ai. Ine ndikufuna kuti iwe ndi Ziba mugaŵane chuma cha Saulo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mfumu inayankha kuti, “Uneneranji zambiri? Ine ndikulamula kuti iwe ndi Ziba mugawane minda.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.