2 Samuel 19:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo anthu adaloŵa mu mzinda kachetechete, monga momwe anthu amaloŵera mu mzinda mwamanyazi, akamathaŵa kunkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kachetechete, monga azemba anthu akuchita manyazi pakuthawa nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo analowa mu mzinda mwakachetechete tsiku limenelo ngati momwe amalowera anthu mwamanyazi chifukwa athawa ku nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo tsiku lija anthu analowa m'mudzi kacetecete, monga azemba anthu akucita manyazi pakuthawa nkhondo.