2 Samuel 19:32 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Barizilai anali munthu wokalamba, wa zaka 80 zakubadwa. Ndipo iye ndiye ankapatsa mfumu chakudya nthaŵi imene mfumuyo inkakhala ku Mahanaimu, pakuti iyeyo anali munthu wolemera kwambiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka chakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsono Barizilai anali wokalamba kwambiri, wa zaka makumi asanu ndi atatu. Iye ndi amene anapereka zinthu kwa mfumu pamene anali ku Mahanaimu pakuti anali wolemera kwambiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Barizilai anali nkhalamba, ndiye wa zaka makumi asanu ndi atatu; ndiye amene anapereka cakudya kwa mfumu muja anagona ku Mahanaimu, pakuti anali munthu womveka ndithu.